Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhulupiriro ndi Kukula

Chikhulupiriro ndi dzanja lolandira malonjezo onse a Mulungu, ndipo moyo wachikhulupiriro uyenera kukula. Baibulo limatiyitana kuti tikhulupirire, timvere, tiyeretsedwe, ndi kupirira mpaka kumapeto. Mavesi awa amadyetsa kuyenda kokhazikika ndi kozama ndi Mulungu — chiyembekezo chogwiritsitsa ndi chisomo chopitirizira.

Chikhulupiriro ndi Kudalira

Chikhulupiriro — Ahebri 11:1

Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.

Kudalira Mulungu — Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

Kudalira Mulungu — Yohane 15:5

“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Kukhulupirira Mulungu — Afilipi 1:6

Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

Kuyenda mwa Chikhulupiriro — 2 Akorinto 5:7

Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.

Chikhulupiriro Ngati cha Mwana — Mateyu 18:3

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

Chikhulupiriro Chopanda Ntchito Ndi Chakufa — Yakobo 2:17

Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Chishango cha Chikhulupiriro — Aefeso 6:16

Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo.

Chikhulupiriro Chimasuntha Mapiri — Mateyu 17:20

Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.

Kukhulupirira Mosaona — Yohane 20:29

Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”

Chikhulupiriro Chimabwera mwa Kumva — Aroma 10:17

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

Wolungama Adzakhala ndi Moyo mwa Chikhulupiriro — Habakuku 2:4

“Taona, mdani wadzitukumula; zokhumba zake sizowongoka, koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.

Ambuye, Kulitsani Chikhulupiriro Chathu — Luka 17:5

Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”

Chiyembekezo ndi Kutsimikizika

Chiyembekezo — Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.

Kutsimikizika kwa Chipulumutso — 1 Yohane 5:13

Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha.

Chiyembekezo Chodala — Tito 2:13

pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,

Chiyembekezo Chokhazikika — Ahebri 6:19

Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga.

Malonjezo a Mulungu — 2 Akorinto 1:20

Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu.

Chiyembekezo Chosakhumudwitsa — Aroma 5:5

Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.

Chiyembekezo mwa Mulungu — Masalimo 42:5

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi

Osungidwa Bwino — Yohane 10:28

Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.

Osungidwa ndi Mphamvu ya Mulungu — 1 Petro 1:5

Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza.

Mphamvu Yatsopano — Yesaya 40:31

koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.

Cholowa Chosungidwa — 1 Petro 1:4

kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba.

Khristu Chiyembekezo Chathu — 1 Timoteyo 1:1

Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.

Kumvera ndi Kudzipereka

Kumvera — Yohane 14:15

“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

Kudzipereka — Aroma 12:1

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Kugonjera Mulungu — Yakobo 4:7

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

Kuwerengera Mtengo — Luka 14:28

“Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?

Kunyamula Mtanda — Mateyu 16:24

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.

Kuchita Chifuniro cha Mulungu — Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.

Kumvera Kuposa Nsembe — 1 Samueli 15:22

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

Osati Chifuniro Changa — Luka 22:42

“Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”

Kudzipereka kwa Mtima Wonse — Mateyu 22:37

Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.

Kuyenda M'njira Zake — Deuteronomo 10:12

Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,

Ochita Mawu — Yakobo 1:22

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Chilichonse Chimene Anena — Yohane 2:5

Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”

Kukula Mwauzimu ndi Kuyeretsedwa

Kuyeretsedwa — 1 Atesalonika 4:3

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama;

Kukula Mwauzimu — 2 Petro 3:18

Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.

Kusinthidwa — 2 Akorinto 3:18

Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

Kukhwima Mwauzimu — Ahebri 6:1

Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,

Uphunzitsi wa Ophunzira — Mateyu 28:19

Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,

Kukonzedwanso — Aroma 12:2

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Kulimbikira Kupita Patsogolo — Afilipi 3:14

Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.

Kulangizidwa ndi Chilango — Ahebri 12:11

Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

Kuchoka ku Mkaka Kupita ku Chakudya Cholimba — 1 Akorinto 3:2

Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe.

Kuvala Munthu Watsopano — Akolose 3:10

ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.

Kufanizidwa ndi Chithunzi Chake — Aroma 8:29

Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri.

Gwirizani Ntchito Chipulumutso Chanu — Afilipi 2:12

Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,

Kupirira ndi Kumaliza Bwino

Kupirira — Yakobo 1:12

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

Kupirira — Ahebri 12:1

Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Kukhazikika — 1 Akorinto 15:58

Choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.

Kuleza Mtima — Aroma 12:12

Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.

Kuthamanga Liwiro — Ahebri 12:1-2

Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.

Kukhulupirika M'zinthu Zazing'ono — Luka 16:10

“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.

Musatope — Agalatiya 6:9

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

Kumaliza Liwiro — 2 Timoteyo 4:7

Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro.

Kuyima Cholimba — Aefeso 6:13

Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu.

Owerengedwa Okhulupirika — 1 Akorinto 4:2

Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika.

Gwiritsitsani — Ahebri 10:23

Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.

Chipewa cha Moyo — Chivumbulutso 2:10

Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.