Mavesi a m'Baibulo Onena za Chiyembekezo Chosakhumudwitsa

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Chiyembekezo Chosakhumudwitsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 5:5

Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.

02 Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo.

03 Masalimo 25:3

Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

04 Yesaya 49:23

Mafumu adzakhala abambo wongokulera ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera. Iwo adzagwetsa nkhope zawo pansi. Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova; iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”

05 Aroma 10:11

Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”

06 Aroma 8:24-25

Pakuti ife tinapulumutsidwa mʼchiyembekezo ichi. Koma chiyembekezo chimene chimaoneka si chiyembekezo ayi. Kodi ndani amene amayembekezera chimene ali nacho kale? Koma ngati ife tiyembekeza chimene tikanalibe, ndiye kuti tikuyembekeza modekha mtima.

07 Afilipi 1:20

Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa.

08 Masalimo 22:5

Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa. Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

09 Ahebri 6:18-19

Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira. Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga.

10 1 Petro 2:6

Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti, “Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni, wosankhika ndi wamtengowapatali. Amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”

Mitu yofanana