Mavesi a m'Baibulo Onena za Chiyembekezo mwa Mulungu

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Chiyembekezo mwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 42:5

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Yembekezera Mulungu, pakuti ndidzamulambirabe, Mpulumutsi wanga ndi

02 Masalimo 42:11

Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

03 Masalimo 39:7

“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani? Chiyembekezo changa chili mwa Inu.

04 Maliro 3:24

Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse; motero ndimamuyembekezera.”

05 Masalimo 130:5

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake.

06 Masalimo 33:20-22

Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu. Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera. Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

07 Masalimo 71:5

Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.

08 Masalimo 62:5

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.

09 Mika 7:7

Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo, ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga adzamvetsera.

10 Masalimo 147:11

Yehova amakondwera ndi amene amamuopa, amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.

11 Masalimo 33:18

Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,

12 Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chiyembekezo adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pamene mukumudalira Iye, kuti chiyembekezo chanu chisefukire mwamphamvu ya Mzimu Woyera.

Mitu yofanana