Mavesi a m'Baibulo Onena za Chiyembekezo Chodala

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Chiyembekezo Chodala oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Tito 2:13

pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,

Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.

03 1 Yohane 3:2-3

Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.” Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

06 1 Yohane 3:2

Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.

07 Afilipi 3:20-21

Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.

08 Akolose 3:4

Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.

09 2 Timoteyo 4:8

Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.

10 Mateyu 24:30

“Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika.

12 Chivumbulutso 1:7

“Onani akubwera ndi mitambo,” ndipo “Aliyense adzamuona, ndi amene anamubaya omwe.” Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.” Zidzakhaladi momwemo, Ameni.

Mitu yofanana