Mavesi a m'Baibulo Onena za Osungidwa Bwino

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Osungidwa Bwino oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 10:28

Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.

02 Yohane 10:29

Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga.

03 Aroma 8:38-39

Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

04 1 Petro 1:5

Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza.

05 Yuda 1:24

Kwa Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe mʼmachimo, ndiponso amene angathenso kukufikitsani pamaso pake pa ulemerero wopanda cholakwa muli okondwa,

06 Deuteronomo 33:27

Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’

07 Masalimo 37:24

ngakhale atapunthwa sadzagwa, pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.

08 Yesaya 41:13

Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.

Mitu yofanana