Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhulupiriro Ngati cha Mwana

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Chikhulupiriro Ngati cha Mwana oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 18:3

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

02 Marko 10:15

Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.”

03 Mateyu 18:4

Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

04 Masalimo 131:2

Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.

05 Mateyu 11:25

Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono.

06 Marko 10:14

Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa.

Mitu yofanana