Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudalira Mulungu
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kudalira Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.
Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,
Ndikachita mantha ndimadalira Inu.
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye. Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu.