Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhulupiriro Chimasuntha Mapiri

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Chikhulupiriro Chimasuntha Mapiri oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 17:20

Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.

02 Marko 11:23

Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.

03 Mateyu 21:21

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.

04 Marko 9:23

Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”

05 Luka 17:6

Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.

06 Mateyu 21:22

Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”

07 Marko 11:24

Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.

08 1 Akorinto 13:2

Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu.

09 Zekariya 4:7

“Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ”

10 Mateyu 9:29

Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.”

11 Afilipi 4:13

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

12 Ahebri 11:33

amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango,

13 Yakobo 1:6

Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo.

Mitu yofanana