Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudalira Mulungu
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kudalira Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu? Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo. Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu.
Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye.
Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.