Mavesi a m'Baibulo Onena za Chishango cha Chikhulupiriro
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Chishango cha Chikhulupiriro oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo.
Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana.
Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.
“Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika; Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo.