Mavesi a m'Baibulo Onena za Chikhulupiriro ndi Kudalira
Chikhulupiriro chimavomereza Mawu a Mulungu ndi kuyika kulemera konse kwa moyo pa Iye. Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luntha lako lomwe. Mavesi awa amalimbikitsa kudalira kotsimikizika, kopuma mwa Mulungu wokhulupirika.
Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.
“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.
Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.
Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo.
Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani.
Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
“Taona, mdani wadzitukumula; zokhumba zake sizowongoka, koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”