Mavesi a m'Baibulo Onena za Wolungama Adzakhala ndi Moyo mwa Chikhulupiriro
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Wolungama Adzakhala ndi Moyo mwa Chikhulupiriro oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Taona, mdani wadzitukumula; zokhumba zake sizowongoka, koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”
Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro. Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha, Ine sindidzakondwera naye.
Abramu anakhulupirira Yehova, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.
Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo.
ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.