Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukhulupirira Mosaona

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kukhulupirira Mosaona oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 20:29

Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”

02 1 Petro 1:8

Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.

03 2 Akorinto 5:7

Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.

04 Ahebri 11:1

Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.

05 Yohane 20:31

Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

06 2 Akorinto 4:18

Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Mitu yofanana