Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudzipereka kwa Mtima Wonse

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kudzipereka kwa Mtima Wonse oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 22:37

Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.

02 Deuteronomo 6:5

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.

03 Yoswa 24:15

Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova.”

04 Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

05 Akolose 3:23

Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.

06 Marko 12:30

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’

07 Masalimo 86:11

Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.

08 1 Mafumu 8:61

Koma mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Yehova Mulungu wanu, kutsatira malamulo ake ndi kumvera malangizo ake, monga lero lino.”

09 2 Mbiri 16:9

Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”

Mitu yofanana