Mavesi a m'Baibulo Onena za Kumvera ndi Kudzipereka

Chikondi cha Mulungu chimadzionetsa mu kumvera kwachimwemwe ndi moyo woperekedwa ku chifuniro chake. Osati kufuna kwanga, koma kwanu kuchitidwe. Mavesi awa amakuyitana kuti utsate kulikonse komwe akutsogolera, ukukhulupirira kuti malamulo ake ndi abwino.

Kumvera — Yohane 14:15

“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

Kudzipereka — Aroma 12:1

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Kugonjera Mulungu — Yakobo 4:7

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

Kuwerengera Mtengo — Luka 14:28

“Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?

Kunyamula Mtanda — Mateyu 16:24

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.

Kuchita Chifuniro cha Mulungu — Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.

Kumvera Kuposa Nsembe — 1 Samueli 15:22

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

Osati Chifuniro Changa — Luka 22:42

“Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.”

Kudzipereka kwa Mtima Wonse — Mateyu 22:37

Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.

Kuyenda M'njira Zake — Deuteronomo 10:12

Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,

Ochita Mawu — Yakobo 1:22

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Chilichonse Chimene Anena — Yohane 2:5

Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”