Mavesi a m'Baibulo Onena za Kumvera

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kumvera oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 14:15

“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

02 1 Samueli 15:22

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

03 Yakobo 1:22

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

04 Yohane 14:23

Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye.

05 1 Yohane 5:3

Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa,

06 Deuteronomo 11:1

Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake.

07 Yoswa 1:8

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

08 Luka 6:46

“Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena?

09 Yohane 15:14

Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani.

Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!

11 Aroma 6:17

Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.

12 1 Petro 1:14

Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa.

13 Deuteronomo 30:16

Pakuti lero ndikukulamulani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kuti muyende mʼnjira zake, ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake. Mukatero mudzakhala ndi moyo ndi kuchulukana, ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukulowa kukakhalamo.

Mitu yofanana