Mavesi a m'Baibulo Onena za Kugonjera Mulungu

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kugonjera Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yakobo 4:7

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

02 Aroma 6:13

Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.

03 Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

04 1 Petro 5:6

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.

05 Aroma 12:1

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Mitu yofanana