Mavesi a m'Baibulo Onena za Chilichonse Chimene Anena

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Chilichonse Chimene Anena oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 2:5

Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”

02 Luka 5:5

Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”

03 Yohane 15:14

Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani.

04 1 Samueli 15:22

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!

06 Deuteronomo 13:4

Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.

07 Yohane 14:23

Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye.

08 Luka 6:46

“Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena?

09 1 Yohane 2:3

Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake.

10 Yeremiya 7:23

koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.

11 Eksodo 19:8

Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.

12 Mateyu 8:27

Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”

13 Yohane 10:27

Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.

14 Masalimo 119:34

Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.

Mitu yofanana