Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyenda M'njira Zake
Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kuyenda M'njira Zake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova. Odala ndi amene amasunga malamulo ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.”
Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.