Mavesi a m'Baibulo Onena za Ochita Mawu
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Ochita Mawu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.
“Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe.
Koma Yesu anayankha kuti, “ Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”
Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.
Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama.
Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.
Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo.
“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.
Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.
Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.