Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukhulupirika M'zinthu Zazing'ono
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kukhulupirika M'zinthu Zazing'ono oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.
“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
“Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli. (“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)
Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.
Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika.
“Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’
“Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.
Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.
Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni?
Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”
Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.