Mavesi a m'Baibulo Onena za Kumaliza Liwiro
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kumaliza Liwiro oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro.
Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.
Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamanga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho.
Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.
Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire.
Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.
Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.
Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota.
Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.