Mavesi a m'Baibulo Onena za Musatope
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Musatope oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
Iye amalimbitsa ofowoka ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.
“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.
Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo.