Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulangizidwa ndi Chilango

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kulangizidwa ndi Chilango oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Ahebri 12:11

Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

02 Ahebri 12:6

Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”

03 Miyambo 3:11-12

Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake. Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

04 1 Akorinto 9:27

Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.

05 Yobu 5:17

“Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.

06 Deuteronomo 8:5

Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.

07 Chivumbulutso 3:19

Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.

Mitu yofanana