Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuyeretsedwa

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kuyeretsedwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Atesalonika 4:3

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama;

02 1 Petro 1:15-16

Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.”

03 Yohane 17:17

Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.

04 Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.

05 2 Timoteyo 2:21

Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

06 2 Atesalonika 2:13

Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.

07 Aroma 6:22

Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.

Mitu yofanana