Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukonzedwanso
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kukonzedwanso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu;
Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano! Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona? Ine ndikulambula msewu mʼchipululu ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.