Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuchoka ku Mkaka Kupita ku Chakudya Cholimba
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kuchoka ku Mkaka Kupita ku Chakudya Cholimba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe.
Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo. Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,
Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo.
Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya.
Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Abale, lekani kuganiza ngati ana. Mukhale ana pa nkhani ya zoyipa koma mʼmaganizo anu mukhale okhwima.
Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.
Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu.
Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba!