Mavesi a m'Baibulo Onena za Uphunzitsi wa Ophunzira

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Uphunzitsi wa Ophunzira oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 28:19

Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,

02 Luka 9:23

Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.

03 Yohane 8:31-32

Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

04 Mateyu 11:29

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

05 Yohane 13:35

Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”

06 Luka 14:27

Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

07 Mateyu 16:24

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.

08 Yohane 12:26

Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.

Mitu yofanana