Mavesi a m'Baibulo Onena za Owerengedwa Okhulupirika
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Owerengedwa Okhulupirika oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika.
“Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake.
“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.
Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena.
“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’
Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo.
Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.
Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu.
Koma sinditero ndi Mose mtumiki wanga; Iyeyu ndi wokhulupirika mʼnyumba yanga yonse.
Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.
Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito.