Mavesi a m'Baibulo Onena za Kufanizidwa ndi Chithunzi Chake
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kufanizidwa ndi Chithunzi Chake oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri.
Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.
Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.
Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu,
ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.
ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.
Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake. Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri.
Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.”
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.
Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.