Mavesi a m'Baibulo Onena za Mphamvu Yatsopano
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Mphamvu Yatsopano oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.
Iye amalimbitsa ofowoka ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka, ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa; koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.
Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.
Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake,
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo. Yehova ndi mphamvu ya anthu ake, linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake.
Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”
Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe
Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga; amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi, amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.