Mavesi a m'Baibulo Onena za Gwirizani Ntchito Chipulumutso Chanu
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Gwirizani Ntchito Chipulumutso Chanu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera,
pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.
Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.
Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine.
Ife tikufuna kuti aliyense wa inu aonetse changu chomwechi mpaka kumapeto, kuti zichitikedi zomwe mukuyembekezera.
Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.
Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu.
Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye.
Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse.