Mavesi a m'Baibulo Onena za Umunthu ndi Moyo Wamkati

Mwa Khristu wapatsidwa dzina latsopano ndi mtima watsopano — wosankhidwa, wokhululukidwa, ndi wokondedwa kwambiri. Malemba amalankhula moona za moyo wamkati: maganizo a mtima, malingaliro a nzeru, ndi nkhondo yopitiriza yolimbana ndi tchimo. Mavesi awa amazikitsa umunthu wako pa zimene Mulungu akunena kuti ndi zoona, osati pa zimene ukumva.

Umunthu mwa Khristu

Mwana wa Mulungu — 1 Yohane 3:1

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

Osankhidwa — Aefeso 1:4

Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,

Wokondedwa — Akolose 3:12

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.

Opambana Koposa — Aroma 8:37

Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.

Omasulidwa — Yohane 8:36

Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu.

Nzika za Kumwamba — Afilipi 3:20

Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu.

Kuwala kwa Dziko — Mateyu 5:14

“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.

Mchere wa Dziko Lapansi — Mateyu 5:13

“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.

Unsembe Wachifumu — 1 Petro 2:9

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

Ntchito ya Manja a Mulungu — Aefeso 2:10

Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

Akazembe a Khristu — 2 Akorinto 5:20

Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

Olandiridwa mwa Wokondedwayo — Aefeso 1:6

Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.

Wopangidwa Mochititsa Mantha ndi Modabwitsa — Masalimo 139:14

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mtima ndi Mtundu wa Maganizo

Nkhawa — Afilipi 4:6-7

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mantha — Yesaya 41:10

Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Kuda Nkhawa — Mateyu 6:34

Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

Chisoni — Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

Kusungulumwa — Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”

Chimwemwe — Nehemiya 8:10

Nehemiya anatinso, “Pitani, kachiteni phwando ku nyumba ndipo mukawagawireko ena amene alibe kanthu kalikonse popeza lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Musakhale ndi chisoni, pakuti chimwemwe cha Yehova ndiye mphamvu yanu.”

Mtendere — Yohane 14:27

Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

Chitonthozo — 2 Akorinto 1:3-4

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.

Kutaya Mtima — Yoswa 1:9

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Manyazi — Aroma 10:11

Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”

Kutaya Mtima — Masalimo 42:11

Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Mtima Wosweka — Masalimo 147:3

Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.

Kusowa Chitetezo — Yeremiya 1:5

“Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale, iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale; ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”

Kuyamika — 1 Atesalonika 5:18

Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

Kuopa Anthu — Miyambo 29:25

Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.

Mkwiyo — Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Maganizo ndi Nzeru

Kukonzanso Maganizo — Aroma 12:2

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Kugwira Ukapolo Maganizo — 2 Akorinto 10:5

Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

Kusinkhasinkha — Masalimo 1:2

Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

Kuika Maganizo Kumwamba — Akolose 3:2

Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.

Kukayika — Yakobo 1:6

Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo.

Chisokonezo — 1 Akorinto 14:33

Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo koma wamtendere. Monga mwa mipingo yonse ya oyera mtima.

Maganizo Abwino — 2 Timoteyo 1:7

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

Lingalirani Zinthu Izi — Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

Maganizo Okhazikika — Yesaya 26:3

Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.

Maganizo a Khristu — 1 Akorinto 2:16

Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu.

Tetezani Mtima Wanu — Miyambo 4:23

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.

Khalani Maso — 1 Petro 5:8

Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.

Ndisanthuleni, Mulungu — Masalimo 139:23

Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.

Tchimo ndi Kulilimbana Nalo

Tchimo — Aroma 3:23

pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu

Thupi — Agalatiya 5:16

Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo.

Chiyeso — 1 Akorinto 10:13

Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.

Kunyada — Miyambo 16:18

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.

Chilakolako — Mateyu 5:28

Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.

Umbombo — Luka 12:15

Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”

Kupembedza Mafano — 1 Yohane 5:21

Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Kuzondana — Ahebri 12:15

Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.

Nsanje — Yakobo 3:16

Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.

Kugonjetsa Tchimo — Aroma 6:14

Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.

Kuvula Munthu Wakale — Aefeso 4:22-24

Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.

Kuthawa Tchimo — 2 Timoteyo 2:22

Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.

Kukana Mdyerekezi — Yakobo 4:7

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

Osakhalanso Akapolo a Tchimo — Aroma 6:6

Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo