Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusowa Chitetezo
Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kusowa Chitetezo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale, iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale; ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.
Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye. Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Koma tsopano, Yehova amene anakulenga, iwe Yakobo, amene anakuwumba, iwe Israeli akuti, “Usaope, pakuti ndakuwombola; Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse.
Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu.
Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,