Mavesi a m'Baibulo Onena za Nkhawa

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Nkhawa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Afilipi 4:6-7

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

02 1 Petro 5:7

Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

03 Mateyu 6:25

“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?

04 Masalimo 55:22

Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

05 Yohane 14:27

Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

06 Masalimo 94:19

Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

07 Miyambo 12:25

Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu, koma mawu abwino amamusangalatsa.

08 Yesaya 41:13

Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.

09 2 Atesalonika 3:16

Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

10 Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.

11 Mateyu 11:28-30

“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Mitu yofanana