Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusungulumwa
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kusungulumwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya Yehova adzandisamala.
Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako, amene ndikukugwira dzanja lako lamanja ndipo ndikuti, usaope; ndidzakuthandiza.
Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.
Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu? Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko. Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja, kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.
Ine ndili nawe pamodzi ndipo ndidzakuyangʼanira kulikonse upiteko, ndipo ndidzakubwezera ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjezazi.”