Mavesi a m'Baibulo Onena za Mtendere
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Mtendere oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.
Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.
Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.
“ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.’ ”
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.
Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo; zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa,
Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.