Mavesi a m'Baibulo Onena za Chitonthozo
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Chitonthozo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.
Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.
Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi: lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
Atonthozeni, atonthozeni anthu anga, akutero Mulungu wanu.
Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.
Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.