Mavesi a m'Baibulo Onena za Khalani Maso

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Khalani Maso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 5:8

Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.

02 1 Atesalonika 5:6

Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga.

03 1 Petro 1:13

Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera.

04 1 Petro 4:7

Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.

05 Tito 2:12

Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,

06 Aroma 13:11-12

Ndipo chitani ichi pozindikira nthawi ino. Nthawi yafika yoti inu mudzuke kutulo, chifukwa chipulumutso chathu chili pafupi tsopano kuposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku watsala pafupifupi kutha. Kwatsala pangʼono kucha. Tiyeni tsono tichotse ntchito zamdima ndipo tivale chovala chakuwunika.

Mitu yofanana