Mavesi a m'Baibulo Onena za Chisokonezo

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Chisokonezo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Akorinto 14:33

Pakuti Mulungu si Mulungu wachisokonezo koma wamtendere. Monga mwa mipingo yonse ya oyera mtima.

02 Yakobo 3:16

Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.

03 Yakobo 1:5

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

04 Yesaya 26:3

Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.

05 Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

06 Yohane 14:27

Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

07 Masalimo 32:8

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.

08 Yeremiya 29:11

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

09 Akolose 2:2-3

Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso.

Mitu yofanana