Mavesi a m'Baibulo Onena za Kugwira Ukapolo Maganizo

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kugwira Ukapolo Maganizo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Akorinto 10:5

Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

02 Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

03 Akolose 3:2

Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.

04 Aroma 12:2

Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

05 Yesaya 26:3

Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.

06 Miyambo 4:23

Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.

07 1 Petro 1:13

Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera.

08 Masalimo 19:14

Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

09 Ahebri 12:2

Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.

Mitu yofanana