Mavesi a m'Baibulo Onena za Kusinkhasinkha

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kusinkhasinkha oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 1:2

Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

02 Yoswa 1:8

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

03 Masalimo 119:15

Ndimalingalira malangizo anu ndipo ndimaganizira njira zanu.

04 Masalimo 19:14

Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

05 Masalimo 143:5

Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita.

06 Masalimo 119:97

Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.

07 Masalimo 63:6

Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.

08 Masalimo 77:12

Ndidzakumbukira ntchito zanu ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

09 Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

10 Masalimo 104:34

Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye, pamene ndikusangalala mwa Yehova.

11 Masalimo 145:5

Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

Mitu yofanana