Mavesi a m'Baibulo Onena za Wokondedwa
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Wokondedwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima. Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.
Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
Za fuko la Benjamini anati: “Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye, pakuti amamuteteza tsiku lonse, ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”