Mavesi a m'Baibulo Onena za Nzika za Kumwamba
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Nzika za Kumwamba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu.
Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu.
Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.
Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.
Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.
Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.
Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.
Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.
kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba.
Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi.
Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba.
Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka.