Mavesi a m'Baibulo Onena za Mwana wa Mulungu
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Mwana wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;
Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,
Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.
Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.
Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.