Mavesi a m'Baibulo Onena za Omasulidwa

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Omasulidwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 8:36

Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu.

02 Agalatiya 5:1

Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.

03 Aroma 8:2

chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.

04 Yohane 8:32

Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

05 2 Akorinto 3:17

Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu.

06 Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi.

07 Luka 4:18

“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,

08 Aroma 6:18

Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.

09 Aroma 6:22

Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.

10 Masalimo 118:5

Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova, ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.

11 1 Akorinto 7:22

Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu.

Mitu yofanana