Mavesi a m'Baibulo Onena za Osankhidwa

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Osankhidwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 1:4

Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,

02 1 Petro 2:9

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

03 Yohane 15:16

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.

04 2 Atesalonika 2:13

Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.

05 Akolose 3:12

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.

06 Deuteronomo 7:6

Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.

Mitu yofanana