Mavesi a m'Baibulo Onena za Unsembe Wachifumu

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Unsembe Wachifumu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 2:9

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

02 Eksodo 19:6

inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”

03 Chivumbulutso 1:6

ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.

04 1 Petro 2:5

inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

05 Chivumbulutso 5:10

Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.”

06 Ahebri 13:15

Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake.

Mitu yofanana