Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuthawa Tchimo

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kuthawa Tchimo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Timoteyo 2:22

Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.

02 1 Akorinto 6:18

Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.

03 1 Akorinto 10:14

Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano.

04 1 Timoteyo 6:11

Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.

05 Genesis 39:12

Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.

06 Miyambo 4:14-15

Usayende mʼnjira za anthu oyipa kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa. Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo; uzilambalala nʼkumangopita.

07 1 Atesalonika 5:22

Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.

08 2 Timoteyo 2:19

Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”

09 Yakobo 4:7

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.

10 Miyambo 5:8

Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo, usayandikire khomo la nyumba yake,

11 Aroma 13:14

Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.

12 1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.

Mitu yofanana