Mavesi a m'Baibulo Onena za Chiyeso
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Chiyeso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo.
Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.
Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.
Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe!